Abambo atatu ali m’chitokosi powaganizira kuti anatentha a Carolyn Suleman, 21, amene akuti anatumiza ndalama zokwana K800,000 kwa munthu osadziwika pa Airtel Money.
Ofalitsankhani pa Polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, ati izi zinachitika Lamulungu ku Malangalanga ndipo amene akuwaganizirawa ndi a Doud Yasin, 38, Francis Sadik, 31 ndi Alfred Phiri, 30.
A Chigalu ati a Suleman analandira thenifolo yachilendo m’mawa ndipo anauzidwa kuti apite pa agent aliyense wa Airtel Money kuti atumize ndalamazo kwa anthu atatu ndipo anatumiza ndi a Yasin, amene amachita malonda awo pa sitolo ya Premier Bet ya Mungo.
Atamaliza kutumiza ndalamazo, a Yasin anamufunsa mtsikanayo kuti awapatse koma iye anati alibe komanso anati samamudziwa munthu amene wamuuza kuti atumize ndalamayo.
Bambowa, pamodzi ndi a Sadik komanso a Phiri, amene amagwiranso ntchito ku Premier Bet komweko, anamutengera ochitidwa chipongweyi m’chipinda chosungirako katundu ndi kumuthira petulo wa mu generator ndi kumuyatsa moto.
Kutsatira izi, a Chigalu anati Carolyn anathamangira naye ku chipatala cha Kamuzu Central kumene akulandira thandizo la mankhwala chifukwa wavulala kwambiri thupi lonse.
Atatuwa akuyembekezeka kuyankha mlandu ovulaza munthu.