Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Apolisi ku Mangochi amanga Boika atam’peza ndi chida choopsya

Apolisi ku Mangochi amanga a Boika Sabiti, 48, atawapeza ndi chida choopsya chopangidwa ndi zitsulo zosongoka komanso zokuthwa.

Ofalitsa Nkhani pa Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, ati a Sabiti adawapeza ndi chidachi pa malo omwela mowa m’boma la Mangochi.

“Tinawuzidwa ndi anthu ena akufuna kwabwino kuti a Sabiti akuyenda ndi chida choopsa chomwe anasunga m’chikwama chomwe amayenda nacho, ndipo ife apolisi tidathamangira kwa Mtalimanja komwe tinawapeza nacho,” a Daudi anatero.

Sabiti, amene amachokera m’mudzi wa Mapira ku Mangochi, ndi kabwerebwere kundende ndipo akaonekela kukhothi kukayankha mulandu opezeka ndi chida chowopsa.

 

Related posts

Chakwera heads to Southern Region for official duties

MBC Online

RA, Stakeholders to relocate Muloza One Stop Border Post

Rabson Kondowe

FAM dates coaches ahead of new season

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.