Malawi Broadcasting Corporation
Education Local Local News Nkhani

Aphungu athandiza ophunzira pa sukulu ya Malingunde

Nyumba ya malamulo yapereka thandizo la zinthu zosiyanasiyana ku sukulu ya ophunzira amene ali ndi ulumali osaona ya Malingunde m’boma la Lilongwe.

Sipikala wanyumbayi, a Catherine Gotani Hara, ndiye amene anatsogolera aphungu pa mwambowu pamene analimbikitsa ophunzira kuti achilimike maphunziro kuti adzathe kukhala nzika zodalirika.

A Hara anati achita izi monga gawo limodzi lazochitika zimene anakonza mu sabata yodziwitsa anthu mmene nyumba yamalamulo imagwilira ntchito zake.

Mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya Malingunde, a Vincent Mathanki, anayamikira aphungu anyumba ya malamulo kaamba kathandizolo.

Iwo anati sukuluyi, imene ili ndi ophunzira 70, imavutika kupeza chakudya chokwanira, komanso zipangizo zophunzilira ana amene ali ndi ulumali osaona (Braille) ndi ochepa.

Mwakatundu amene aphungu anapereka ndi chimanga, mafuta, zovala, ndowa ,mpunga, ndi zina zambiri zimene zinakwana K9 million.

Related posts

Ritz Attorneys at Law empowers MUBAS law program.

Alinafe Mlamba

Ndife okondwa kuti boma limatiika mmapulani ake – Ras Mwanamanga

Mayeso Chikhadzula

Local chiefs, subordinates nabbed over chieftaincy wrangles

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.