Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Amumanga ku Kamuzu Central chifukwa chakuba mankhwala

Apolisi ku Lilongwe agwira a Chikumbutso Ngilazi amene amagwira ntchito ku chipatala cha Kamuzu Central powaganizira kuti akhala akuba mankhwala a nkhaninkhani.

Malinga ndi ofalitsankhani wa apolisi ku Lilongwe, a Hastings Chigalu, a Ngilazi, amene ndi a zaka 34, akukhudzidwa ndi nkhani yakubedwa kwa mankhwalawa amene apolisi adapeza ku Mpanipani mumsika wa Lilongwe.

Kumeneku, apolisi adamanga a Hardson Mulenga a zaka 65 ndi mwana wawo wamkazi Regina Stander wa zaka 31, amene amagulitsa mankhwala osiyanasiyana a chipatala popanda chilolezo.

Atamanga anthuwa, apolisiwa akhala akufufuza kumene anthuwa amapeza mankhwalawa ndi pamene akwanitsa kumanga Ngilazi, yemwe amagwira ntchito yothandizira kuchipinda chogawa mankhwala, Pharmacy mchingerezi.

Mkuluyu, kwa zaka khumi ndi ziwiri, amagwira ntchito yochapa ndi kusita pa chipatalachi koma kwa chaka chimodzi anali akugwira ntchito ku Pharmacy ngati wothandizira.

Ngilazi wavomera kuti ndiye wakhala akugulitsa mankhwala wosiyanasiyana kwa a Stander kwa chaka, omwe nkuphatikizapo panadol, amoxicillin, buffen ndi ena ambili.

Malinga ndi a Chigalu, Ngilazi amachokera pamudzi wa Mgawa mdera la mfumu Mlolo m’boma la Nsanje ndipo akaonekera kubwalo la milandu posachedwapa kumene akayankhe mlandu wakuba mankhwala munthu wogwira yotumikira anthu m’boma.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

Silver Strikers near unbeaten first round

MBC Online

A Ken Msonda alowa chipani cha MCP

Chisomo Manda

Malawi Fertilizer Company itha kupanga fertilizer okwana 150, 000 tons

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.