Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local News

Alipire chindapusa chifukwa chotchula mzake kuti mfiti

Khoti la Midima ku Limbe mumzinda wa Blantyre lalamula mayi Veronica Chakhumbira  azaka 34 kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana K30, 000 chifukwa chotchula mzake kuti ndi mfiti pa masamba a mchezo.

Wachiwiri kwa ofalitsankhani zapolisi ku Limbe, Chibisa Mulimbika, wati mayi Chakhumbira analemba pa Facebook kuti mzawoyo ndi mfiti ndipo atawerenga, mzake wamayiyo anakanena izi ku polisi ya Bangwe ndipo apolisiwo anachenjeza mayiyo kuti alekeretu mchitidwewu.

Koma mayiyo anapitirizabe kutchula mayi mzakeyo kuti ndi mfiti, zomwe zinachititsa kuti apolisiwo amumange.

Mayi Chakhumbira ndi wa mmudzi wa Nkhanyanga, mfumu yaikulu Changata ku Thyolo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Malawi suffers second defeat

Romeo Umali

K90 million lost to vandalism-ESCOM

Davie Umar

Alimi ndi okhutira ndi kampani zogula fodya

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.