Pofuna kuonetsetsa kuti ana, achikulire komanso okalamba akulandira thandizo lachipatala mwaulemu komanso mogwirizana ndi ufulu wawo akapita kuchipatala, bungwe la masisiteli ampingo wa Katolika la Association of Women in Religious Institute of Malawi (AWRIM), kudzera mu AWRIM Health Care Network, lachititsa maphunziro a masiku awiri kwa anthu ogwira ntchito m’zipatala za mpingowu.
Maphunzirowa amapereka upangiri wa momwe angathandizire odwala omwe ali pa chiopsyezo. Maphunzirowa anachitikira mu mzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi a Sisiteli Teresa Mulenga omwe akuyendetsa ntchitoyi pansi pa bungwe la AWRIM Health Care Network , nthumwi zomwe zinabwera pa maphunzilowa zikuyembekezeka kukagawana ndi kuphunzitsa anzawo m’zipatala zonse za mpingo wa Katolika m’zigawo zonse dziko lino.
“Taphunzila zambiri monga kulemekeza odwala komanso momwe tingawathandizire malinga ndi ufulu wawo”, anatero Sisiteli Mulenga.
Sisiteli Mulenga anatinso pamaphunzirowa anabweretsa anthu omwe amagwira ntchito za kalembera mzipatalazi kuti adzitha kupanga kalondolondo wa bwino wa anthu omwe umoyo wawo uli pa chiopsyezo.
Mmodzi mwa nthumwi za kumaphunzirowa Sisiteli Lexina Mwale omwe alikuchipatala cha Ludzi ati maphunzirowo ndi ofunika kwambiri ndipo abwera mu nthawi yake.
“Taphunzira zothandiza kwambiri anthu amene miyoyo yawo ili pa chiopsyezo monga ana ndi anthu achikulire komanso okalamba,” anatero Sisiteli Mwale.
Wolemba Glory Chinyanga
#MBCDigital
#Manthu

