Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Wapha mwana wa zaka zitatu chifukwa chodutsa mmunda mwake

Apolisi ku Chiradzulu amanga John Tebulo wazaka 43 pomuganizira kuti wapha mwana wazaka zitatu kaamba kodutsa mmunda mwake.

Ofalitsankhani wapolisi ku Chiradzulu, Cosmas Kagulo, wati makolo a mwanayo analawilira kumunda kumusiya akugona kaamba koti mundawo unali pafupi.

Atadzuka, mwanayo anayamba kulondola makolo akewo ndipo anadutsira m’munda mwa Tebulo.

Izi sizinamusangalatse ndipo anatenga chikwanje ndikuyamba kukhapa mwanayo, yemwe anthu anathamangira naye kuchipatala koma mwatsoka, anali atamwalira.

Apolisi apulumutsanso woganiziridwayo kaamba koti anthu ammudzi anayamba kumumenya moti akulandira thandizo kuchipatala atavulala kwambiri.

Izi zachitika m’mudzi wa Likhomo, mfumu yaikulu Sandrack m’boma la Chiradzulu.

 

Olemba: Charles Pensulo

Related posts

CICOD, others empowers women, youth in agriculture

Romeo Umali

SFFRFM for quality, affordable fertilizer

Romeo Umali

Mlingo wa kukwera mtengo kwa zinthu (inflation) watsika mu February

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.