Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News

Tizidziwa zotsatira za kafukufuku — MPUC

Bungwe loona zachitetezo ndi umodzi m’dziko muno la Malawi Peace and Unity Commission (MPUC) lapempha mabungwe komanso adindo kuti adzichita changu pofufuza nkhani komanso kubweretsa zotsatira zake poyera.

Wapampando wa bungwe la MPUC, a Mary Mkosi, ati kuchita motero kuthandiza kuti anthu omwe salemekeza malamulo a dziko la Malawi adzionekera ng’amba komanso adzilangidwa.

A Mkosi anapemphanso a Malawi kuti adzilemekeza mabwalo a milandu maka nthawi yomwe mabwaalowaakupanmga chigamulo.

Iwo amanena izi mu mzinda wa Lilongwe pamsonkhano wa olembankhani omwe cholinga chake unali kuwunikira zina mwandondomeko zabungweli.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

SAPP-MALABO INTERVENTIONS ENDING MALNUTRITION IN CHILDREN

MBC Online

Chakwera holds successful bilateral talks with UAE leadership

MBC Online

Big Brother Naija returns

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.