Bungwe la Malawi Red Cross Society (MRCS) lati lamaliza ntchito yogawa ndalama kwa mabanja amene anakhudzidwa ndi namondwe Judy m’boma la Phalombe m’chaka cha 2023.
Mabanjawa ndi oposa 1,000 ndipo alandira K140,000 komanso sopo ochapira ndi osambira banja lililonse.
M’modzi wa akuluakulu ku bungweli, a Leanord Maganga, ati ali ndi chikhulupiliro kuti anthuwa agwiritsa ntchito ndalamazi moyenera.
“Takhutira ndi momwe ntchitoyi yayendera. Posachedwapa, ma voluntiya athu akhala akuyendera mabanjawa kuti awone momwe agwiritsire ntchito ndalamazi,” a Maganga anatero.
Mmodzi mwa anthu omwe alandira nawo ndalamazi, a Alex Nkhoma, athokoza bungwe la Red Cross kaamba ka thandizoli, ponena kuti tsopano apeza pogwira.
Ndondomekoyi yagwiridwa ndi ndalama zokwanira K550 million m’ma boma a Mulanje, Chikwawa ndi Phalombe.


