Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

ESCOM yayamika Chakwera chifukwa cha $21 million

Kampani ya Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM) yati $21 million yomwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chalwera anakatenga ku msonkhano wa COP27 ithandizira kugulira zida zamakono zosungira mphamvu ya magetsi a dzuwa.
‎
‎Izi zikudza pamene kampani za ESCOM ndi Electricity Generation Company (EGENCO) zikufunitsitsa kuonjezera mphamvu zamagetsi m’dziko muno popeza kampanizi zataya magetsi ambiri kaamba ka umbava wazida zofunikira.
‎
‎Mkulu wa EGENCO, a Maxon Chitawo, wati chidwi chawo chili pofuna kupanga mphamvu zamagetsi zosachepera 2000 megawatts pofika chaka cha 2040.

A Chitawo ati, pakadali pano, bungweli likukumana ndi mikwingwirima monga ngozi zakudza kaamba kakusintha kwa nyengo komanso kuwonongeka kwa makina opangira mphamvu zamagetsi ku Kapichira, Nkula komanso Tedzani.
‎
Iwo ati dongosolo lokhazikitsa malo atsopano opangira mphamvu zamagetsi m’ma boma a Salima ndi Nkhotakota liri m’chimake.
‎
‎Pakadalipano, dziko la Malawi linamaliza ntchito yonse yofuna kutenga mphamvu zamagetsi zokwana 50 megawatts kuchokera m’dziko la Mozambique kumene kwatsala kuti amalizitse.
‎

Related posts

MRA hails One-Stop Border Posts as revenue game changer

McDonald Chiwayula

Three Mozambicans nabbed for possessing ivory without licence

Romeo Umali

We need more banking halls in Malawi — Tchereni

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.