Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Chakwera ndi namandwa — Msungama

Phungu wanyumba ya malamulo wadera la Lilongwe City South East, yemwe pano akufuna kudzayimira dera la Lilongwe Mlodza, a Ulemu Msungama, wayamikira mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, chifukwa cha ndalama zimene amapereka ku thumba la Community Development Fund (CDF), zimene anati zathandizira kuti zitukuko zidzichitika.

“President Chakwera adaonjezera ndalama mu thumba la CDF mwadaladala, pofuna kuti phungu aliyense agwire ntchito zomwe anthu ake akuzifuna ndipo zimenezi zathandiza kuti madera ambiri atukuke. Ndikofunika kuti aMalawi tidziyamika,” a Msungama anatero.

Iwo amayankhula izi pamene iwo pamodzi ndi akuluakulu ochokera ku khonsolo ya nzinda wa Lilongwe amakhazikitsa ntchito yomanga mlatho umene uli ku Don Bosco munzindawu.

Mlathowu ndi omwe umalumikiza madera a Ngwenya ku Area 24 ndi Area 23.

Kampani ya Urban and Rural Group Limited ndi imene imange mlathowo ndipo ntchito yonse ikuyembekezeka kutha m’miyezi itatu.

A Msungama anapempha amene akugwira ntchitoyi kuti agwire mwadongosolo ndi cholinga chakuti mlathowu ukhale olimba komanso wamakono.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Malawi joins Tanzania in celebrating 60th Anniversary

Arthur Chokhotho

Govt optimistic about reviving international agro-business deals

Earlene Chimoyo

Parliament passes the Cannabis Amendment Bill

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.