Nthambi ya boma yoyang’anira mabungwe a masewero yati bwalo la makono la masewero la BAT lomwe boma likumanganso mu mzinda wa Blantyre muzidzalowa anthu okwana 17 000.
Mkulu wa nthambiyi, Dr Henry Kamata, anauza olemba nkhani momwe ntchitoyi ikuyendera yomwe akuti chigawo choyamba chatha pamene amagumula ndi kusalaza pamalopa.
Iwo ati bwalo latsopanoli lidzakhala ndi denga ku ma stand onse ndipo akulimanga motsatira ndondomeko zovomerezeka za masewero osiyanasiyana.
A Kamata ati Bwaloli likhala ndi ma ofesi a ogwira ntchito za masewero komanso ma ofesi ena omwe azidzabwereketsa kwa anthu ochita malonda.
Pali chiyembekezo choti bwaloli likatha, lizidzapeza ndalama kuchokera ku ofesi zake pobwereketsa ndipo lidzakhala lodzidalira palokha pa chuma kuchokera ku ndalama za ofesizi.
Olemba: Amin Mussa
#MBCDigital
#Manthu