Unduna waza malonda ndi mafakitale walamula kuti m’mwenye yemwe anatsekula shopu yake ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe, momwe amagulitsa zinthu za hardware, akhale atatseka shopu yake pasanathe masiku 14.
Malinga ndi chikalata chomwe wasayinila m’modzi mwa akuluakulu ku unduna waza malonda, a Ezron Chirambo, m’mwenyeyu sakuyenera kuchita bizinesi yake kumsika wa Nsungwi.
Masiku apitawa, mavenda wogulitsa zinthu za hardware ku Nsungwi anatseka sitolo ya m’mwenyeyu pokwiya naye kamba koti amasokoneza malonda awo chifuwa mpamba wawo sukugwirizana ndi mapezedwe am’mwenyeyo, yemwe akuti amaphangira bizinesi pogulitsa mwachipiku komanso pang’onopang’ono katundu yemwe amapanga yekha.
Prezidenti wabungwe la Black indigenous business Network a Kate Kamwangala ati zomwe boma lachita pa nkhaniyi zaonetsa kudzipereka kwake polimbikitsa a bizinesi zing’ono zing’ono mdziko muno.
M’neneli wa mavenda aku Nsungwi, a Albert Zuwawo, wayamika boma chifukwa choonetsetsa kuti abizinesi zing’ono zing’ono m’dziko muno sakuphinjika.