Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Development Local Local News Nkhani

AGCOM ikutukula alimi

Bungwe la Agriculture Commercialisation (AGCOM) lathandiza kutukula gulu la alimi limene akulitcha kuti ‘Team North Cooperative’ lochokera ku Lupaso munzinda wa Mzuzu.

Poyankhula pamene nduna ya zamalonda ndi mafakitale, a Sosten Gwengwe, inayendera gulu la alimiwa, wapampando wa gululi, a Chimwemwe Sibale, anati anayamba ndi alimi khumi m’chaka cha 2018.

A Sibale anati pano ali ndi alimi 56 ndipo chaka chino alima mtedza pa hekitala 35 ndi soya pa ma hekitala 100 komanso misika anayipeza kale m’dziko la Kenya ndi ku kampani zina m’dziko muno.

A Gwengwe analimbikitsa alimiwa kuti adzilima zochuluka ndi kusankha bwino ndi kuyika zokolola zawo m’ma paketi ochititsa kaso.

Kuposera apo, ndunayi inatinso ndi pofunika kuti alimi adzipanga zinthu zina kuchokera ku mbewu zimene akulima kuti adzipeza phindu lochuluka.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Maintain human agency at centre of technological advancements – DC

MBC Online

Sports analyst urges Malawi Beach Soccer to utilise home ground

Romeo Umali

Temwa Chawinga makes history as NWSL MVP

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.