Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Likhutcha alimbikitsa bata

Mkulu waza chipembedzo kulikulu la apolisi mdziko muno ku Area 30, Bambo mfumu Steven Likhutcha wapempha a Malawi onse kuti agwilane manja panthawi yomwe dziko lino likukhuza maliro a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndi anthu ena asanu ndi atatu omwe adafa pa ngozi ya ndege.

Poyankhula pa mwambo woperekeza matupi a asilikali a Malawi Defence Force (MDF) komanso apolisi awiri ndi dotolo wa malemu Dr Chilima ku Sunset Funeral Services ku Kanengo, a Likhutcha apempha a Malawi kuti apewe mchitidwe wolembankhani komanso kulankhula zinthu zomwe anati zingapomboneze anthu m’dziko muno.

Naye mlangizi wa Prezidenti pa nkhani ya zipembedzo, m’busa Brian Kamwendo, wapempha atsogoleri amipingo kuti akhale patsogolo polimbikitsa umodzi pakati pa a Malawi onse panthawi ya zovutazi.

Mwambowu inatsogolera ndi nduna yazofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, omwe anali limodzi ndi nduna zina za boma komanso mlembi wamkulu ku ofesi ya Prezidenti ndi Kabineti a Colleen Zamba.

Related posts

Alimi asamale pogula mbewu — Self Help Africa

Romeo Umali

Abwezedwa ndi komiti

Rabson Kondowe

Ntchito yoponya voti ili mkati ku ward ya Mwasa

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.