Malawi Broadcasting Corporation
Local News

Tiyeni tigwirizane pokonda dziko – Chaponda

Mtsogoleri  wa zipani zotsutsa kunyumba ya malamulo, a George Chaponda, wati ali ndi chisoni  chifukwa cha imfa ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Malemu Dr Saulos Chilima.

Poyankhula ndi MBC ku siwa ku Area 12 mu mzinda wa Lilongwe, a Chaponda anati  Malemu  Dr Chilima akhala akugwira ntchito yotamandika  potumikira a Malawi ndi boma.

Mwazina, a Chaponda apempha a Malawi kuti agwirane manja ndi boma panthawi ya zovutayi ponena kuti maliro sazolowereka.

Akulu akulu a zipani zosiyanasiyana, kuphatikizapo aphungu akunyumba ya malamulo, ali kunyumba ya siwayi.

 

Related posts

Sho Madjozi to perform at 2024 Lake of Stars Arts festival

Romeo Umali

ActionAid hands 12 motorcycles to health project partners

Rabson Kondowe

Kalindo has a case to answer

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.