Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News

Ntchito yonyamula zovuta ku Chikangawa yayambika

Apolisi limodzi ndi azachipatala ayamba kunyamula matupi a anthu amene ataya miyoyo yawo pangozi ya ndege imene yagwa chapa Lunjika mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Chilima pamodzi ndi akuluakulu ena asanu ndi anayi, apezeka atamwalira pa ngoziyi, malinga ndi kutsimikiza kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pamene amayankhula kwa mtundu wa Malawi.

Pakali pano, matupi a anthuwo akuyembekezeka kutengedwa kuchoka ku nkhalangoyi kupita ku Capital Hill munzinda wa Lilongwe.

Akuluakulu aboma, aphungu aku nyumba ya malamulo komanso makhansala ndi anthu osiyanasiyana ali pamalowa, pamene asilikali a dziko lino akuyesetsa kukhazikitsa bata ndikutsogolera anthu mwadongosolo pa malowa.

Olemba: Jackson Sichali

Related posts

Four nabbed for commiting various crimes in Mzimba

Rabson Kondowe

Italy channels €4 million via WFP to feed school children in Chikwawa

McDonald Chiwayula

BANKING AMENDMENT BILL NEEDS FURTHER CONSULTATIONS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.