Malawi Broadcasting Corporation
Tourism

Zokopa alendo sikunyanja kokha – Kamtukule

Unduna woona zokopa alendo m’dziko muno wati uli pakalikiliki kuphunzitsa anthu kuti asinthe kaganizidwe pa nkhani ya zokopa alendo.

Nduna yoona zokopa alendo, a Vera Kamtukule, anena izi pamwambo olandira cheke cha ndalama zokwana K18 million zoti zithandize pa chiwonetsero cha zokopa alendo cha chaka chino.

“Ambiri amaona ngati zokopa alendo ndi kupita kumalo ogona alendo apamwamba kapena ku nyanja pomwe sichoncho. Iyi ndintchito yomwe tayika pamtima kuti anthu amvetsetse tikamati zokopa alendo ndi chani,” atero a Kamtukule.

A Kamtukule ati magule ngakhalenso kuyenderana ndi mbali imodzi ya zokopa alendo.

A Temwa Kadzanja, omwe ndi mmodzi mwa akuluakulu ku kampani ya Sunbird, ati ndalamayi ithandiza theka la thumba la chuma lomwe boma lakonza pa nkhani ya chakudya cha alendo.

Chiwonetserochi, chomwe cholinga chanke ndikufuna kukweza chuma cha dziko lino podzera mu zokopa alendo, chichitika kuyambira pa 25 mpaka pa 27 April 2024.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

JICA impressed with KIA operations

Lonjezo Msodoka

Malawi, Mozambique agree to strengthen trade ties

MBC Online

Lake Malawi Biomass Trawl Survey Episode 1

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.