Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Unduna waza Malimidwe uyamba kupanga mbewu posachedwapa

By Isaac Jali

Nduna ya zamalimidwe a Roza Mbilizi, yati boma ndi lokhumudwa ndi kukwera mtengo kwa mbewu zomwe zachititsa kuti alimi ena adzale mbewu yosakhala bwino chifukwa cholephera kugula mbewu yabwino.

A Mbilizi anena zimenezi ku Lilongwe pa msonkhano waukulu wa pachaka wa bungwe la alimi ang’onoang’ono la NASFAM.

Iwo anati pofuna kuthana ndi vutoli, unduna wawo uyamba kupanga mbewu yomwe ikhale yotsika mtengo pofuna kuthandiza alimi ambiri omwe sangakwanitse mbewu yomwe makampani akupanga.

“Tikukambirana ndi kampani kuti ziganizirepo zotsitsa mtengo wa mbewu, komabe ngati boma tiyamba kupanga mbewu yathu kuti tithandize alimi ambiri,” atero a Mbilizi.

Iwo anati boma lilimbikitsanso ntchito za ulangizi komanso kuzindikiritsa alimi ubwino ogwiritsa ntchito feteleza wa organic monga wa mbeya pofuna kubwezeretsa chonde mthaka.

Pa nkhani ya ulimi wa khasu, iwo anati nkofunika kuti tsopano alimi athandizidwe kuti ayambe kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono monga ma tractor.  Iwo ati kwa zaka zambiri tsopano, zaonekeratu kuti ulimi wa khasu sukuthandiza kwenikweni kotero nkofunika zipangizo zamakono.

A Mbilizi alimbikitsanso alimi ang’onoang’ono m’dziko muno kuti akhale mmagulu kapena kuti makopaletivi chifukwa ntchito ya AIP iyika chidwi chake kwa alimi omwe ali mmagulu.

M’mau ake, mkulu wa bungwe la NASFAM, a Betty Chinyamunyamu, apempha boma kuti lionetsetse kuti mu ntchito ya fetereza otsika mtengo, ndalama zina zidzipitanso ku mbewu zomwe zingathandize kubweretsa ndalama zakunja, osati chimanga chokha.

Pamwambowo, bungwe la NASFAM lapereka mphatso komanso kufunira zabwino a Mbilizi kaamba kosankhidwa kukhala nduna ya zamalimidwe yoyamba yachizimayi kuyambira pomwe dziko la Malawi lidalandira ufulu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Kafukufuku wati kulorena kwakula m’boma la Mangochi

Davie Umar

All set for UDF Convention

Chisomo Break

National Bank yapanga phindu lokwana K71.96 billion chaka chatha

Justin Mkweu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.