Banki ya National yapanga phindu lokwana K71.96 billion, boma litadulapo kale msonkho mu chaka cha 2023.
Phinduli lakwera poyerekeza ndi phindu la K45.9 billion limene adapeza mu chaka cha 2022.
Izi ndi malinga ndi kalata yazachuma yomwe banki yi yatulutsa.
Bankiyi yati phinduli ladza chifukwa chakuti ndalama zimene anthu amasungitsa ku bankiyi zinachuluka, zomwe zinapangitsa kuti apereke ngongole zambiri.