Akuluakulu ogwira ntchito za umoyo ku ofesi ya Mangochi apempha magulu akufuna kwabwino kuti agwire ntchito limodzi ndi ofesiyi pothandiza kupititsa patsogolo ntchito zaumoyo pakati pa anthu omwe akulandira thandizo la chipatala.
Pempholi ladza pamene gulu la apolisi lotchedwa Mangochi Women Police Network lapereka thandizo losiyanasiyana kuphatikizapo chakudya kuchipinda cha ana operewera zakudya nthupi komanso chipinda cha anthu odwala chifuwa chachikulu.
Malingana ndi wapampando wa Mangochi Women Police Network, Sub Inspector Suzan Msongole, thandizoli ndi limodzi mwa ntchito zachifundo zomwe apolisiwa amagwira pofikira anthu omwe ndi ovutika.
Wina mwa katunduyu ndi sopo, mafuta ophikira shuga komanso ufa.
Olemba Owen Mavula