Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Dr Joyce Banda, wapempha a Malawi kuti adzikamba zinthu zabwino zokhudza dziko lino kuti lipite patsogolo.
Dr Banda, omwe ndi mtsogoleri wa chipani cha PP, amayankhula izi pa msonkhano omwe anachititsa pa bwalo la Nancholi m’boma la Blantyre.
Iwo ati aMalawi ambiri akugwiritsa ntchito masamba a mchezo molakwika ponyoza dziko lino, zomwe ati ndi zomvetsa chisoni.
Mtsogoleriyu watinso mavuto a dziko lino kuti athe akufunika m’gwirizano pakati pa boma, zipani za ndale komanso mabungwe omwe si aboma.
Dr Banda anamemanso a Malawi kuti apitilire kugwira ntchito molimbika ndi cholinga chotukula miyoyo yawo.
Olemba: Blessings Cheleuka
#MBCDigital
#Manthu