Bungwe la Standing Voice lapempha aMalawi kuti achilimike pothandiza kuthetsa nkhanza zomwe anthu ena amachitira anthu achialubino pomaimba lamya ku ma nambala awulele, kupereka uthenga akaona nkhanzazi.
Ma nambalawo ndi 4293, 116, 5600 ndi 6600.
Atsogoleri a bungweli, limene limalimbikitsa ufulu wa anthu a chialubino, anena izi pa misonkhano yomwe akhala akuchita limodzi ndi bungwe la YONECO m’boma la Mulanje ndi cholinga chophunzitsa anthu za ufulu wa anthuwa.
Mabungwewoo akugwira ntchitoyi limodzi ndi apolosi komanso nthambi ya boma yoona zachisamaliro cha anthu.