Mphunzitsi wa timu yaikulu ya dziko lino ya The Flames, Patrick Mabedi, wati anyamata ake akonzeka kuthambitsa timu ya Burkina Faso mawa pa masewero olimbirana malo ku mpikisano wa maiko a muno mu Africa wa Africa cup of Nations.
Mabedi wayankhula izi m’dziko la Mali komwe kuchitikire masewerowa.
“Anyamata akuonetsa chidwi chofuna kupambana ndipo akudziwa kufunikira kotenga mapointi onse pamasewerowa. Tingopempha aMalawi atikhulupilire komanso atiikize mumapemphero kuti tipambane,” watero Mabedi.
Flames inagonja masewero ake oyamba ndi timu ya Burundi pakhomo ndipo pakadali pano ili pansi pa mndandanda wa matimu anayi mugulu lawo, lomwe likutsogozedwa ndi timu ya Senegal yomwe masanawa yagonjetsa Burundi ndi chigoli chimodzi kwa chilowere kuti itenge ulamuliro wa gululi ndi mapointi anayi.