Nduna yoona za chilengedwe, a Michael Usi, yauza akuluakulu osiyanasiyana ogwira ntchito za kafukufuku zokhudza nsomba kuti agwiritse ukadaulo wawo ndi kuonetsetsa kuti achitapo kanthu poonjezera chiwerengero cha nsomba ndi kuonetsetsa kuti m’malawi aliyense akuzipeza pa mtengo otsika.
Ndunayi yanena izi ku Bingu International Convention Centre pa zokambirana zokhudza mmene ndondomeko za nsomba zomwe anakhazikitsa zotchedwa National Plan of Action for Small Scale Fisheries zikuyenera kugwilira ntchito.
A Usi apemphanso a zakafukufukuwa kuti aonetsetse kuti zotsatira zakafukufuku yemwe amachita zikupezeka, akuzigawa komanso akuzigwiritsa ntchito kuti cholinga chake chopindulira dziko lino chikwaniritsidwe.
Iwo ati kwa nthawi yaitali, dziko lino lakhala likungokamba ndi kuchita kafukufuku koma osachitapo kanthu ndipo ati akufuna kuti akuluakuluwa achitepo kanthu kuti aMalawi apindule popeza nsombazi mosavuta komanso motsika mtengo.
Ndunayi yati ili ndi chiyembekezo kuti zomwe atakambirane pa msonkhanowu zipereka mndandanda wa zomwe aliyense atachite pokwaniritsa izi osati kungoyankhula chabe.