Nthambi yowona zolowa ndikutuluka m’dziko muno ya Immigration yati sizoona kuti chiphaso cholowera ndikutulukira m’dziko muno chikhala ndi masamba ochepa komanso chidzitha mu zaka zisanu.
Poyankhula ndi MBC, mneneri wa nthambiyi, a Wellington Chiponde, ati izi ndizabodza ndipo apempha a Malawi kuti asazitengere.
Iwo ati masamba a chiphasochi akadali monga analili kale ngakhale atsitsa ndalama zopezera chiphasochi.
A Malawi tsopano adzilipira K50,000 yokha popeza chiphasochi, m’malo mwa K90,000.
Masiku apitawa, anthu ena akhala akufalitsa pa masamba a mchezo kuti boma lachepetsa masamba a chiphasochi komanso zaka zomwe chidzikhalira ndi mphamvu.