Bungwe la NOCMA lati kuyambira sabata ya mawa sitima yonyamula mafuta a galimoto okwana malita 1.2 million iyamba kulowa m’dziko muno kudzera panjanji yochoka ku Beira m’dziko la Mozambique kufika ku Marka m’boma la Nsanje.
Wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la NOCMA a Micklas Reuben anena izi pa mwambo wopereka uthenga okhudza ngozi za mafuta komanso sitima kwa anthu okhala m’madera oyandikana ndi malo osungira mafutawa ku Kanengo mu nzinda wa Lilongwe.
Bungweli linachititsa msonkhanowu kutsatira mchitidwe opopa mafuta mu sitimayi omwe achinyamata ena okhala mderali akuchita.
A Reuben ati izi zikupereka chiopsezo cha imfa komanso ngozi.
Iwo ati pomwe akuonjezera chiwerengero cha mafuta olowa mdziko muno kudzera pa njanji ndi pofunika kuti anthu akhale ozindikira za kuopsa kwa mafuta komanso sitima.
M’mawu ake phungu wa dera la Lilongwe City Centre a Alfred Jiya ati ndiokhumudwa ndi mchitidwe wu. A Jiya ati agwira ntchito ndi achitetezo kuti aonetsetse kuti achinyamatawa omwe akumagona moyandikana ndi malowa achoke.
Malinga ndi bungwe la NOCMA, kufikira pano dziko lino lalowetsa malita 33 million a mafuta a galimoto kudzera pa njanji.