Bungwe la Roads Authority (RA) lati pamene nyengo yamvula yayamba lionetsetsa kuti misewu komanso milatho yomwe yaonongeka yakonzedwa.
Mneneri ku bungweli, a Portia Kajanga, ayankhula izi atalandira chikalata cha madadandaulo kuchokera kwa Nthanda Khumbanyiwa amene anamang’ala za vuto la kuonongeka kwa misewu komanso milatho ya m’chigawo cha kummwera.
A Kajanga ati ntchito ya bungweli ndi kukonza zinthu monga misewuyi ngakhalenso milatho, choncho awonetsetsa kuti akaona zimene zili mu kalatayi ayankhe moyenera poti ati akhala akuyankha mavuto amene anthu a m’chigawochi akukumana nawo.
Mu chikalatacho, Nthanda wadandaula ndi kuonongeka komanso kuchedwa kukonza kwa misewu ya Sidik Mia Highway, Gwanda Chakwamba Highway komanso milatho ya Miseu Folo, Mtaya Moyo ndi Chapananga imene anati ndi yofunika kwambiri kwa anthu okhala m’chigawochi.
Iye wati anthu a m’chigawochi ndi odandaula kuti pamene nyengo ya mvula ikuyandikira, misewu komanso milatho imene amayidalira pa malonda ngakhalenso kunyamula zinthu zofunika monga mankhwala ndi zina, zinakali zoonongeka.