Osewera wa Premier Bet Dedza Dynamos, Promise Kamwendo, wapempha amene amamutsatira kuti ayiwale zam’mbuyo pa nkhani imene inawutsa mapiri pachigwa posachedwapa atachita mgwirizano osatsatira malamulo ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers m’malo mwa timu ya FCB Nyasa Big Bullets.
Iye anavomereza kuti anaalakwitsa koma wati zimenezi sizinamusokoneze m’kaganizidwe ndipo wayika chidwi chake chonse kuti alimbikire kumwetsa zigoli ku timu ya Premier Bet Dedza Dynamos ndipo ali kale ndi zigoli zisanu ndi zitatu.
Kamwendo amayankhula izi lachitatu atabwelera ku timu yake yakaleyi kutsatira kulamulidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi (FAM) kuti atero.
Mphunzitsi wa Dynamos, a Andrew Bunya, anati ndi okondwera kuti Promise wabwerera chifukwa ndi osewera wawo.
Lachitatu, Kamwendo anali limodzi ndi osewera anzake pamene amachita zokonzekera kuti athambitsane ndi timu ya Creck Sporting Loweruka likudzali.