Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yati yapereka kalata ku nthambi yoona zolowa komanso kutuluka m’dziko muno, zofuna kupeza chilolezo kuti katswiri wawo wakutsogolo ochokera ku Cameroon, Sama Tanjong, ayambe kusewera m’dziko muno.
Tanjong, yemwe posachedwapa wasayina contract yazaka ziwiri ndi Wanderers, analephera kupezeka pamasewero atimuyi ndi FCB Nyasa Big Bullets kaamba kakuti alibe chilolezo chogwira ntchito mdziko muno.
Mkulu wa Wanderers, Panganeni Ndovi, watsimikiza kuti pali kuthekera kuti osewerayu apezeka pamasewero atimuyi kumathero asabatayi
Tanjong, yemwe anayambila mpira wake ku timu yachisodzera ya First Sport ku Cameroon, wasewerako matimu amayiko a Democratic Republic of Congo ndi South Africa, ndipo wagoletsa zigoli 112.
Wolemba: Praise Majawa