Komiti ya kunyumba ya malamulo yowona za chisamaliro cha anthu yati dziko lino likufunika thumba lapadera loyendetsera mikumano komanso ntchito za nyumba yamalamulo ya ana achichepere posadalira mabungwe okha.
Wapampando wa komitiyi, a Savel Kafwafwa, ndi amene anayankhula izi Lachisanu masana m’boma la Salima pa msonkhano otseka zokambirana za aphungu akunyumba ya malamulo ya ana achichepele m’bomalo.
A Kafwafwa anati izi ziyenera kudzera kunyumba yamalamulo komanso ma khonsolo a m’mizinda chifukwa kutero zithandizira kuti ntchito zamtunduwu zizipitililabe ngakhale kuti mabungwe ena atamaliza ntchito zawo.
Mlembi ku unduna oona za chisamaliro cha anthu, a Nwazi Mnthambala, anati ndi zofunikadi kuti zokambirana za ana zamtunduwu zikhazikike mu ndondomeko za boma zomwe zilipo kuti ntchitoyi ikhazikike m’dziko muno.