Pali nkhawa kuti kuchepa kwa mlingo wa cocoa yemwe amalimidwa m’maiko amene ali kuchigawo cha kumadzulo kwa Africa kupangitsa kuti mitengo ya chokoleti padziko lonse ikwere.
Maiko a Ghana ndi Ivory Coast amalima 60% ya cocoa pa dziko lonse, ndipo maiko awiriwa akhala akukumana ndi mavuto pa ulimiwu.
Malipoti akuti m’dziko la Ghana, minda yoposa 590,000 hectares ya cocoa yakhudzidwa ndi nthenda yotchedwa “swollen foot” yomwe imayamba kaye yachepetsa zokolola, isanapheletu mitengo ya cocoa.