Sukulu ya luso lamanja ya Mzuzu ili pachiopsyezo chosatsegulira mwezi wa mawawu kaamba ka ngongole yoposa K65 million imene ili nayo.
Mkulu wa sukuluyi, a Julius Phiri, wanena izi pomwe nthambi yakunyumba yamalamulo imene imalondola ndalama zaboma ya Public Accounts Committee (PAC) imakumana mu mzinda wa Mzuzu.
“Pamwezi timayenera tilandire ndalama yoposa K10.5 million. Takhala tikutenga ngongole komanso kulephera kubweza ngongole ku makampani amene amatigulitsa zinthu zoyendetsera sukulu kuphatikizapo chakudya,” iwo anatero.
Wapampando wa PAC, a Mark Botoman, anati ndi okhumudwa chifukwa sukulu yokhayo imene ikusula luso la ntchito zamanja ku Mzuzu ikukumana ndi mavuto azachuma mpaka kufuna kuyitseka.
“Ife ngati komiti yakunyumba yamalamulo tiyankhulana ndi akuluakulu aku unduna wazachuma kuti ndalama zifike mwansanga pa sukulu pano,” a Botoman anatero.
Boma limathandiza sukulu ya Mzuzu Technical College. M’mbuyomu, a mpingo wa Katolika nawonso ankhathandizira koma anasiya.