Osewera kutsogolo wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Patrick Mwaungulu, amupatsa nambala 11 yomwe adzivala pa Malaya ake a timuyi.
Izi zadziwika mu chikalata chimene atulutsa a timu ya Bullets pamene amatulutsa m’ndandanda wa osewera a timuyi mu chaka cha 2024.
Mwaungulu amusintha kuchoka pa nambala 29 yomwe amupatsa Chawanangwa Gumbo, amene poyamba amavala nambala 31.
Osewera ena monga Clyde Senaji, Richard Chimbamba, Yankho Singo, Kenneth Pasuwa ndi Ephraim Kondowe nawonso awasinthira nambala zawo.