Amene akonza phwando la mayimbidwe la Ku Mingoli Bash achotsa oyimba onse akunja monga Cassper Nyovest ndi Young Stunna pam’ndandanda wa oimba akuphwando la chaka chino.
A Shadreck Kalukusha, amene akuyendetsa phwandoli, ati pakadali pano chidwi chili kwa oyimba aku Malawi amene ati akufuna kuti adziwalemekeza powalipira bwino ndi kuwapatsa zoyenera.
“Tikufuna tipange zosiyana chaka chino, khama limene timayika pa oyimba monga Busy Signal akabwera tiliyike pa Tay Grin kapena Namadingo,” anatero a Kalukusha.
Phwando la Ku Mingoli Bash ndi lachiwiri kuchitika chaka chino pomwe oyimba 27 a m’dziko muno adzayimbe patsikuli m’mwezi wa August pa bwalo la Civo munzinda wa Lilongwe.