M’busa wa mpingo wa Salvation for All Ministries International, a Clifford Kawinga, wati njira yomwe akugwiritsa ntchito yogawa chimanga ndi katundu akamalalikira ikuthandiza kwambiri pa cholinga chawo chofuna kutumikira anthu m’dziko muno kuthupi ndi ku uzimu komwe.
A Kawinga anena izi ku Salima m’dera la mfumu yaikulu chotaika komwe anagawa matumba a chimanga kwa anthu 3,000 omwe ochuluka mwa iwo ndi okalamba komanso aulumali.
A Kawinga aperekanso mabaibulo kwa mafumu 212 ozungulira delari.
Iwo apemphanso anthu onse m’dziko muno kuti aleke kuchitira nkhanza anthu achikulire koma ati azipereka chikondi kwa anthu oterewa powafikira ndi zosowa zawo.
Mfumu yaikulu Chotaika inayamikira a Kawinga kaamba koperea thandizoli.
Iwo ati njala m’dera lawo yafika pobvuta ndipo apempha enanso akufuna kwabwino kuti nawo achitepo kanthu.