Chipani cha Malawi Congress (MCP) chati ndikofunika kuti chipani chilichonse m’dziko muno chidzilemekeza ufulu wa demokalase komanso kuchita misonkhano mwa mtendere ndi bata.
Mlembi wamkulu wa MCP, a Richard Chimwendo Banda, amayankhula izi Lachisanu mu nyumba ya malamulo munzinda wa Lilongwe pamene amayankha pempho la mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma, a George Chaponda.
A Chaponda anapempha boma kuti lilowerelepo kuti pasadzakhale zipolowe pa msonkhano umene akonza a chipani cha Democratic Progressive munzinda wa Mzuzu komanso wa MCP ku Ekwendeni m’boma la Mzimba.
A Chimwendo Banda anati chipani chawo sichifuna zipolowe ndipo anati palibe vuto kuti zipani ziwiri zichititse msonkhano kaamba kakuti malo amene kukachitikire misonkhanoyo ndi otalikana makilomita 21.