Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

Matimu 24 amu Tambala Super Cup alandira zawo

Matimu 24 amu chikho cha Tambala Super cha m’boma la Blantyre alandira ndalama zawo kuchokera kwa othandiza chikhochi a Amazon Group of Companies.

Awa ndi matimu amene amaliza pa nambala yoyamba mpakana yachitatu muzigawo zawo zimene amasewera masewero awo mu chikhochi.

Matimu asanu ndi atatu (8) amene anamaliza pa nambala yoyambirira m’zigawo zawo alandira K250,000, amene anathera pachiwiri apochera K150, 000 ndipo iwo amene anathera pa nambala yachitatu alandira ndalama zokwana K100,000 aliyense.

Ma timu awiri amene amaliza pa mwamba mu gawo iliyonse ndi amene afika mu ndime ya ma timu 16 yomwe ikuyamba Lamulungu, pa 17 November 2024.

Mkulu wa kampani ya Amazon, a Mosess Kunkuyu, amenenso ndi nduna yofalitsa nkhani, anati ndi okondwa kuti chikhochi chayenda bwino kufikira mu ndimeyo.

Iwo anatinso ndi okhutira ndi momwe ma timu asewelera.

Mlembi wa komiti yoyendetsa masewero a mpira wamiyendo m’boma la Blantyre, a Sadati Bonzo, ati ndime yomaliza ya mpikisanowu idzakhalapo mu sabata yachiwiri ya mwezi wa December chaka chomwechino.

Chikho cha Tambala Super Cup, chimene ndi cha ndalama zokwana K10 million, anachikhazikitsa m’mwezi wa August ndipo matimu 90 aku Blantyre ndi amene akhala akupikisana.

Olemba: Amin Mussa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHAKWERA ATTENDS CHANCELLOR’S DAY

MBC Online

Charcoal producers clash with forest rangers

Romeo Umali

Balaka SDA delivers a message of peace to the sick

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.