Nduna yowona za mphavu yamagetsi, a Ibrahim Matola, lero ayendera ntchito yolumikiza magetsi kumadera akumudzi yotchedwa Malawi Rural Electrification Program – MAREP phase 9 kumadera a Choma ku Mzimba ndi Ruviri komaso Chozoli m’boma la Rumphi.
Ntchitoyi yomwe yafika gawo lolumikiza ma transformer ithandizira zipatala, sukulu, mabizinesi ndi nyumba za anthu omwe akukhala madera akumudzi komwe sikunafike magetsi.
A Matola alimbikitsa mafumu ndi anthu awo kuti asamalire chitukukochi kaamba koti boma lalowetsa ndalama zambiri powonetsetsa kuti midzi yonse ikhale ndi magetsi mdzikomuno
Group Village Elton Zika Chimaliro omwe akuyimilira midzi yokwana zisansu ndi ziwiri -12 yomwe itapindule ndi ntchitoyi , ati tsopano ndiwokondwa popeza poyamba analibe chiyembekezo kuti magetsiwa atha kufika ku dera kwawo.
Iwo ati akuyembekezera kuti izi zithandizira kuti ana a sukulu azichita bwino pa maphunziro awo.
Olemba Yamikani Makanga