Komiti yoona za matenda a Covid 19 siyidayankhulepo kanthu pambuyo pa malipoti osonyeza kuti munthu m’modzi wapezeka ndi nthendayi m’boma la Mangochi.
Malinga ndi mmodzi mwa madotolo apachipatala chachikulu cha Mangochi, Innocent Lanjesi, mayi wazaka 32 mdera lamfumu yaikulu Makanjira ku Mangochi wapezeka ndimatenda a COVID 19.
Iwo ati izi zadziwika pamene madotolo osiyanasiyana ali mderali kuthandiza anthu ochokera mmadera akutali oti sangakwanitse kukafika kuchipatala chachikulu cha Mangochi.
Madotolowa ali ku Makanjira ndibungwe lachifundo laku German la Hilal Africa.
MBC Digital inayesayesa kufuna kumva kuchokera kwa akuluakulu a COVID-19 Committee komanso ku unduna wa zaumoyo amene panthawiyo samapezeka.
Dr. Lanjesi ati panopa mayiyu amutumiza kuchipatala chachikulu cha Mangochi kukalandira thandizo.