Gulu la amayi ochita mapemphero a pachaka la Women’s World Day of Prayer la m’chigawo chapakati lapereka thandizo lokwana K5.5 million kwa ana aulumali pa sukulu ya pulayimale ya Salima LEA komanso chipatala cha bomalo.
M’modzi mwa akuluakulu a gululi, a Tracy Massi, ati amayiwa achita izi pofuna kuchepetsa mavuto omwe malo awiriwa akukumana nawo.
A Massi ati iwo alimbikitsa amayi m’dziko muno kuti akhale patsogolo pogwira ntchito zachifundo kuti athe kusintha miyoyo ya anthu ena amene ndi ovutika.
Mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi, a Nathan Sambo, anati ana amene amaphunzira pa sukuluyi amachokera m’maboma ambiri komanso amasowa thandizo la zinthu zofunikira pa moyo wawo.
Ndipo m’modzi mwa akuluakulu apa chipatalachi, a Silvia Kandiyesa, anathokoza amayiwa pa thandizoli ndipo anati pamalowa pamafika odwala amene amakhalitsa, zomwe zimachititsa kuti avutike kwambiri.
Matumba a chimanga ndi mpunga, sopo osambira ndi ochapira, shuga, mafuta ophikira ndi zovala ndi zina mwa katundu amene alandira anthuwa.