Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Gulu la alimi lapeza K620 million kudzera mu ulimi wa nzimbe

Cooperative ya Salima Cane Growers yati pofika pa 30 September chaka chino, inakwanitsa kupeza ndalama zoposa K620 million kuchokera ku ulimi wa nzimbe itagulitsa nzimbe zoposa matani 8.8 million m’chaka cha ulimi cha 2023/2024.

Wapampando wa gululi, a Dennis Mpota, ati izi zachitika kaamba ka thandizo la ndalama zokwana K162 million kuchokera ku bungwe lopititsa patsogolo ulimi la Agricultural Commercialisation (AGCOM).

“Ndalamazi tinagwiritsa ntchito pogula tractor yomwe ikutithandiza kulima ma hekitala ambiri kuposera kale komanso galimoto lonyamula katundu (Truck) yomwe ikumanyamula nzimbe za alimi,” atero a Mpota.

Poyankhula itayendera malowa ndi kuchita mwambo wopereka zipangizozi, nduna ya zaulimi a Sam Kawale yati masomphenya a boma ndi ofuna kuti alimi ang’onoang’ono ayambe kuchita ulimi wa bizinesi komanso wogwiritsa ntchito makina ndi zipangizo zina zothandiza pa ulimi osati makasu.

Ndipo mfumu yaikulu Makanjira ya mdelari yayamikira mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, pokhazikitsa mfundo zothandiza kudzutsanso ulimi zomwe akuti zithandiza kuti chuma cha dziko lino chikwere.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Court grants stay order on release of Chinese involved in Wildlife Crimes and Money Laundering

Mayeso Chikhadzula

Police arrest 18 in Balaka

Romeo Umali

Insufficient funding crippling Chess popularity — CHESSAM

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.