Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Dziko la Malawi lili ndi mwai waukulu woonjezera Mphamvu zamagetsi

Nduna yoona zamphamvu zamagetsi, a Ibrahim Matola, yomwe imachita nawo msonkhano waukulu wamaiko apa dziko lonse wokambirana zamphamvu zamagetsi wa World Energy Congress ku Rotterdam mdziko la Netherlands, yati msonkhawu ndi wofunika kwambiri ku dziko la Malawi.

A Matola ati zomwe akambirana ku msonkhawu zikugwilizana ndi masomphenya a mtsogoleli wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, woonetsetsa kuti dziko la Malawi likupanga mphamvu zamagetsi zochuluka.

Iwo anati masomphenya a Malawi 2063 sangakhale atanthauzo popanda kulimbikitsa ntchito yoonetsetsa kuti mdziko muno magetsi alipo okwanira.

Mwazina, a Matola anati nkofunikanso kuti achinyamata akhale patsogolo kuthandiza pa nkhani yamphamvu zamagetsi pogwiritsa ntchito njira zamakono.

Iwo anati makampani ambiri akunja ali ndi chidwi chodzayambitsa ntchito zamphamvu zamagetsi komanso za zamigodi ndi zina m’dziko muno.

Ku msonkhawu, omwe udayamba pa 22 April ndipo utha pa 25 April, 2024 kwafika nthumwi zoposa 7000 komanso nduna zamaiko osiyanasiyana 70 ndipo zikukumbirana pamutu wokonzanso ndondomeko poonetsetsa kuti anthu apa dziko lonse akhale ndi mwayi wamphamvu zamagetsi.

Pafupifupi anthu 18 mwa anthu 100 alionse mdziko muno ali ndi mwayi wokhala ndi mphamvu zamagetsi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

SAUDI ARABIA AFRICAN LEADERS SUMMIT ON – KUNKUYU

MBC Online

CHINA PLEDGES CONTINUED SUPPORT TO MALAWI

MBC Online

SENIOR CHIEF KUNTAJA EXALTS CHAKWERA LEADERSHIP

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.