Bungwe la Central Region Water Board (CRWB) lapereka mphoto kwa ena mwa makasitomala ake omwe amalipira madzi mokhulupirika.
Cholinga cha mphotozi ndi kufuna kulimbikitsa anthu ena, zimene akuti zikhoza kuthandiza kukweza ndi kupititsa patsogolo ntchito yogawa madzi chigawo chonse chapakati.
Ofalitsankhani ku CRWB, a Zephelino Mitumba, ndi amene ananena izi pa mwambowo umene umachitikira pa bwalo la masewero la Dowa Community m’boma la Dowa.
Iwo anati pali mavuto ambiri amene amakumananawo pa ntchito yopereka madzi, zimene zimachititsa kuti masiku ena madzi asamatuluke m’mipopi.
Makasitomala makumi atatu ndi amene alandira mphoto pa mwambowo.