Magulu okwana 844 osunga ndi kuchulukitsa ndalama pansi pa bungwe la COMSIP Cooperative Union Limited ayamba kulandira thandizo la ndalama zogulira zipangizo za ulimi monga mbewu ndi fetereza.
COMSIP yaika padera ndalama zokwana K2.6 biliyoni zomwe zikuthandiza ma membala ake kuti athe kuchita ulimi wa phindu kudzera mu ntchito yotchedwa Legumes Enterprise Structured Programme (LESP).
Mmodzi mwa omwe apindula ndi ntchitoyi, Lawrence Banda wa gulu la Chisomo m’dera la Mfumu yaikulu Wimbe ku Kasungu, wayamikira ntchitoyi ponena kuti yathandiza kuthana ndi njala komanso kukweza chuma cha mamembala omwe atenga nawo gawo mu ntchitoyi.
“Ndi pulogalamu ya LESP, tapeza matumba awiri a fetereza omwe tagwiritsa ntchito kupanga matumba 10 a feteleza wa Mbeya. Izi zatipatsa chiyembekezo chodzapeza zokolora zochuluka kuti tithane ndi njala ndikupeza ndalama zothandizira pakhomo,” atero a Banda.
Mayi Geremina Chiwaula a ku cluster ya Mbalame mdera la Mfumu yayikulu Dzoole, awuza MBC kuti ali okonzeka kuyamba nyengo ya ulimi wa 2024/25 chifukwa ali ndi makilogalamu 15 a mbewu ya chimanga ndi fetereza wokwanira pa malo a maekala awiri omwe alima.
Mlangizi wa bungwe la COMSIP ku Dowa, Rabecca Munthali, wati kuyambira pomwe ntchitoyi inayamba m’bomali mchaka cha 2022, yasintha miyoyo ya ambiri moti ena akumanga nyumba zapamwamba, kugula ziweto, kulipira maphunziro a ana awo, kuyambitsa mabizinesi, komanso kukhala ndi chakudya chokwanira.
Mkulu woyendetsa ntchito ya LESP ku bungwe la COMSIP, Febron Mwiba, wati maanja okwana 27,321 ochokera ku magulu 844 osunga ndi kuchulukitsa ndalama ndi omwe anaonetsa chidwi cholowa nawo mu ntchitoyi popereka 30 percent ya mtengo wa zipangizo zomwe akugula.
“Bungwe la COMSIP lathandiza maguluwa ndi gawo losaposera theka la ndalama zomwe amafuna kugulira zipangizo za ulimi monga mankhwala ophera tizilombo toyambitsa matenda, fetereza, mbewu yapamwamba komanso zipangizo zina. Tikulimbikitsanso maguluwa kugwiritsa ntchito njira zaulimi zothandiza kuchepetsa mavuto a kusintha kwa nyengo monga kupanga ndi kugwiritsa ntchito fetereza wa Mbeya yemwe amabwezeretsa nthaka komanso kusunga chinyezi,” atero Mwiba.
COMSIP Cooperative Union Limited ndiyo idzagule zokolola za maguluwa komanso kuwapezetsa misika ina komwe angagulitse zokolora zawo pa mitengo yabwino.
Pakadali pano, magulu omwe alowa nawo mu ntchitoyi m’maboma a mchigawo chakum’mwera alandira kale zipangizo zawo za ulimi ndipo maboma khumi ndi asanu (15) mdziko muno ndiwo akupindula ndi ntchitoyi yomwe ikulandira thandizo kuchokera ku bungwe la World Bank ndi thumba la ndalama zochokera ku maiko ndi mabungwe osiyanasiyana lothandiza pa ntchito za mthandizi.