Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News

Chiwerengero cha ngozi za njinga za moto chakwera

Nthambi ya Road Traffic and Safety Services yati chiwerengero cha imfa za ngozi za njinga za moto chakwera poyerekeza ndi zaka za m’mbuyomu.

Mkulu wa nthambiyi, a Christopher Kuyera, wanena izi Lolemba pa msonkhano odziwitsa anthu za chitetezo cha pa msewu mu mzinda wa Lilongwe.

A Kuyera anati ngozi zimene zimakhudza oyendetsa njinga zamoto zinakwera kuchoka pa 726 m’chaka cha 2024 kufika pa 813 m’chaka cha 2025, pomwe anthu omwe anamwalira anachuluka kuchoka pa 145 kufika pa 162.

Kotero, adindo a nthambiyi alimbikitsa oyendetsa njinga za moto za kabaza kuti adzitsatira malamulo apa msewu, a Road Traffic Act ya chaka cha 1997, pofuna kuchepetsa ngozi ndi imfa.

Msonkhanowu anawukonza ndi a bungwe la Riders for Health mothandizana ndi bank ya FDH pansi pa mutu okuti: “tiyeni tipange mayendedwe a kabaza ku khala otetezedwa”.

Mtsogoleri wa Riders for Health m’dziko muno, a Lucy Chiyenda, anati bungweli likufuna kuthandiza pa ntchito yolimbikitsa chitetezo cha pa msewu.

A Chiyenda anati izi ndi zotheka potengera luso limene bungweli lili nalo pogwiritsa ntchito njinga za moto, zimene akuti zidzathandiza kuteteza umoyo wa anthu oyendetsa njinga zamoto mogwirizana ndi unduna wa zaumoyo

Wapampando wa bungwe la akabaza m’dziko muno, a Moses Mwalabu, atsindika kuti bungweli lipitiriza kudziwitsa akabaza za kufunika kotsatira malamulo a pamsewu komanso kulembetsa njinga zawo

Wolemba: Chrissy Mwale

Related posts

‘Sankhani moyenera zokaphunzira ku university’

MBC Online

Kaonga bails out 52 needy students

McDonald Chiwayula

ULAMA COUNCIL SUPPORTS MUSSA’S MOVE TO MCP

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.