Malawi Broadcasting Corporation
Education Local Local News Nkhani

Boma limanga sukulu zamkombaphala zokwana 150

Mlembi wamkulu mu unduna oona zokuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi ndi zosamalira anthu, Dr. Nertha Semphere Mgala, wati boma kudzera mu undunawu limanga sukulu zamkombaphala zokwana 150 ndi thandizo lochokera ku bank yaikulu padziko lonse.

Iye amayankhula mdera la mfumu yaikulu Mtonda m’boma la Mangochi kumene amatsegulira sukulu yamkombaphala imene bungwe la Yamba Malawi lamanga ndi thandizo lochokera ku National Bank.

“Boma lili ndi chidwi chachikulu kuti ana achichepere adzidutsa ku sukulu zamkombaphara asanayambe maphunziro a purayimale kuti adzikonzekeletsa ubongo wawo,”.iwo anatero, uku akuthokoza bankiyi poyika chidwi pamaphunziro a ana.

Ofalitsankhani ku National Bank, Akossa Hiwa, anati bankiyi yagwiritsa ntchito ndalama zokwana K137 million kumangira sukulu zinayi m’maboma a Mangochi, Lilongwe ndi Mzimba.

Dziko la Malawi lili ndi sukulu zovomerezeka zamkombaphala zokwana 13,000.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

District councils urged to enforce spatial plans for development

Austin Fukula

Mfumu yayikulu Mwirang’ombe yayamikira sukulu ya ntchito zaluso lamanja ku Karonga

MBC Online

KATSONGA  COURTS UNCDF ON INVESTMENT OPPORTUNITIES

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.