Gulu lina la a Malawi omwe akudzitchula kuti Mzika Zokhudzidwa ladzudzula mchitidwe wa zipani zina zandale zimene zikufuna kukakamiza bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti lisinthe ndondomeko yogwiritsa ntchito chiphaso cha unzika pa chisankho cha chaka chamawa.
Malinga ndi wapampando wa gululi, a Agape Khombe, malamulo a dziko lino akufotokoza momveka bwino kuti kulembetsa mkaundula wa mavoti pakufunika chiphaso chaunzika ndipo anatsindika kuti mmalawi aliyense okonda dziko lake sangatsutsane ndi mfundoyi.
A Khombe ati monga mzika zokhudzidwa, gulu lawo likudabwa kuti ena omwe akutsutsa za nkhaniyi ndi aphungu amene anakhazikitsa nawo lamuloli kunyumba yamalamulo.
Pamenepa, akuluakulu agululi, omwe anatsogozedwa ndi a Billy Malata, akuti a Malawi azindikire kuti chisankho ndi chinthu chofunika kuchiteteza poonetsetsa kuti mzika zokha zadziko lino ndizo zikuponyadi voti.