Mtsogoleri wa zipani zotsutsa kunyumba ya malamulo, a George Chaponda, wati ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Malemu Dr Saulos Chilima.
Poyankhula ndi MBC ku siwa ku Area 12 mu mzinda wa Lilongwe, a Chaponda anati Malemu Dr Chilima akhala akugwira ntchito yotamandika potumikira a Malawi ndi boma.
Mwazina, a Chaponda apempha a Malawi kuti agwirane manja ndi boma panthawi ya zovutayi ponena kuti maliro sazolowereka.
Akulu akulu a zipani zosiyanasiyana, kuphatikizapo aphungu akunyumba ya malamulo, ali kunyumba ya siwayi.

