Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Politics Uncategorized

MAFUMU ATENGE MBALI POTHETSA NJALA M’DZIKO MUNO

 

Nduna ya maboma ang’ono a Richard Chimwemdo Banda yalangiza mafumu kuti adzionetsetsa kuti pali chilungamo pothandiza anthu a m’midzi.

A Chimwendo Banda omwenso ndi mkulu owona za achinyamata m’chipani cha Malawi Congress (MCP) ati izi zili chomwechi kaamba kakuti mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ali ndi khumbo lothetsa njala m’dziko muno.

“Sizoyenera kuti mabanja okhaokhawo azipindula ndi thandizo lobwelera mudzi wonse,” iwo anafotokozera khwimbi la anthu lomwe linali pa msonkhano omwe umachitikira pa sukulu ya pulayimale ya Nanguwo kwa mfumu yayikulu Chisamba m’boma la Salima.

Pa msonkhanowu agawiranso anthu matumba a chimanga pofuna kuthetsa njala m’derali.

M’mawu ake, Phungu wa dera lapakati pa Boma la Salima a Gerald Kapiseni Phiri anayamikira mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pokhala ndi mtima wa mlerakhungwa.

Olemba: Mayeso Chikhadzula.

#mbconlineservices

Related posts

WHO warns against falsified medication

Romeo Umali

Dr Chakwera calls for faith in nation-building

MBC Online

Ulendo wotsiriza wa Dr Chilima wayambika kupita ku Nsipe

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.